Chikalata Cha Mgwirizano Chofotokoza Za Ufulu Wa Chibadwidwe Wa Munthu
Aliyense
Chidavomerezedwa ndi kulengezedwa ndi msonkhano waukulu mu mfundo 217A (III)
ya pa 10th December, 1948.
Mau Otsogolera
Popeza kuzindikira kuti kudzilemekeza ndi kufanana kwa anthu pa chibadwidwe
ndiwo maziko aufulu, chilungamo ndi mtendere pa dziko lapansi,
Popeza kusalabadira ndi kunyoza ufulu wa munthu kwachititsa mchitidwe wa
nkhaza womwe wakhumudwitsa chikumbumtima cha anthu, ndipo kukhazikitsa kwa dziko
m'mene anthu adzasangalale ndi kulankhula za kukhosi ndiponso kukhulupilira
mopanda mantha ndi kusowa kwalengezedwa ngati chinthu cha mtengo wapatali
chimene anthu wamba amalakalaka.
Popeza nkofunikira ngati munthu saumilizidwa kutero, ngati chinthu chamapeto,
kugaukira ulamuliro wankhanza ndi kuponderezedwa, kuti ufulu wa munthu
utetezedwe ndi malamulo,
Popeza nkofunikira kupititsa mtsogolo ubale wa pakati pa maiko,
Popeza anthu a mu bungwe la mgwirizano wa maiko (United Nations) m'chikalata
chawo (Charter of United Nations) anatsikimikizira chikhulupiliro chawo mu
ufulu wa munthu ndi kusasiyanitsa pakati pa mwamuna ndi mkazi ndiponso
atsimikiza kupititsa mtsogolo chikhalidwe cha anthu ndi umoyo wao,
Popeza maiko mgwirizano alonjeza kukwaniritsa mogwirizana ndi bungwe la
mgwirizano wa maiko (United Nations) kupititsa mtsogolo kulemekeza ndi kutsatira
malamulo a ufulu wa munthu,
Popeza kumvetsetsa ufulu umenewu nkofunika kwambiri kuti lonjezo limeneli
likwaniritsidwe,
Choncho, tsopano,
Msonkhano, Waukulu,
ukulengeza malamulo omwe ali m'chikalata cha mgwirizano chofotokoza za ufulu
wa chibadwidwe wa munthu aliyense ngati muyeso wa chikwaniritso kwa anthu onse
ndi maiko onse, pachifukwa ichi aliyense ndi bungwe lililonse m'dziko,
poganizira za chikalatchi, lidzayesetsa pophunzitsa, maphunziro ndi njira zina
zotsogola kupititsa mtsogolo kulemekeza ufulu wachibadwidwe ndi ufulu wina
m'dziko kudzanso pakati pa maiko, poonetsetsa kuti mfundozi zikuzindikiridwa
ndiponso kutsatidwa pakati pa anthu ndi maiko a mu mgwirizano ndi anthu a
m'madera amene maikowo akulamulira.
Ndime 1
Anthu onse amabadwa aufulu ndiponso ofanana mu ulemu ndi ufulu wao.
Iwowa ndi wodalitsidwa ndi mphamvu zoganiza ndi chikumbumtima ndipo achitirane
wina ndi mnzake mwaubale.
Ndime 2
Aliyense ali ndi ufulu wa chibadwidwe ndi ufulu wina omwe walembedwa
m'chikalata chino, mosasiyanitsa m'mjira iliyonse monga mtundu, maonekedwe a
khungu, mwamuna kapena mkazi, chiyankhulo, chipembedzo, ndale kapena maganizo
ena, dziko lochokera kapena chikhalidwe, katundu ndi chuma, kubadwa kapena
m'mene munthu alili.
Poonjezerapo pasakhale kusiyanitsa poganizira ndale, malamulo kapena m'mene
dziko kapena dera lomwe munthu akuchokera lilili, kaya ndi loima palokha,
lodalira ena, losadzidalira, kapena lomwe likupingidwa m'njira zina.
Ndime 3
Aliyense ali ndi ufulu kukhala ndi moyo, mtendere ndi chitetezo chathupi.
Ndime 4
Palibe munthu amene adzasungidwe mu ukapolo kapena mwaukapolo; ukapolo ndi
malonda a akapolo adzathetsedwa m'njira zonse.
Ndime 5
Palibe amene adzachitiridwe nkhaza kapena kuzunzidwa kapena kupatsidwa
chilango monyozedwa.
Ndime 6
Aliyense ali ndi ufulu kuzindikiridwa ngati munthu kulikonse pamaso pa
lumulo.
Ndime 7
Aliyense ndi ofanana pamaso pa lamulo ndipo ali oyenera kutetezedwa
mosasiyanitsa ndi lamulo. Aliyense ali oyenera kutetezedwa ku tsankho la
mtundu uliwonse lomwe likututsa chikalata chino kudzanso kuyambitsa tsankho
lililonse la mtundu wotere.
Ndime 8
Aliyense ali ndi ufulu wolandira chithanzizo chokwanira ndi bwalo la milandu
lodalirika pa zochita zophwanya ufulu wa munthu womwe waperekedwa kwa iye ndi
malamulo a dziko.
Ndime 9
Palibe amene adzamangidwe, kusungidwa osazengedwa mlandu kapena kuumirizidwa
kuchoka m'dziko lake mosatsatira lamulo.
Ndime 10
Aliyense ali ndi ufulu womveredwa mosasiyanitsa ndi bwalo la milandu loyima
palokha ndipo losakondera, poganizira ufulu wa munthu ndi udindo wake ndiponso
mlandu uliwonse womukhudza.
Ndime 11
- Aliyense wozengedwa mlandu asaganiziridwe kuti ndi wolankwira lamulo ndipo
asam'zenge mlandu potsatira malamulo ena amene ali ovomerezeka m'dzikomo
kapena pakati pa maiko, koma omwe pa nthawi yolakwirayo sanali ovomerezeka.
- Chimodzimodzinso chilango chokhwima kuposa chomwe chidalipo panthawi
yolakwira lamuloyo chisaperekedwe.
Ndime 12
Palibe amene adzasokonezedwe chinsinsi chake, banja lake, kwawo, kapena
makalata ake, kapena zochitika zina zoyenera pa ulemu ndi mbiri yake.
Aliyense ali ndi ufulu kutetezedwa ndi lamulo ngati zoterezi zichitika.
Ndime 13
- Aliyense ali ndi ufulu kuyenda ndi kukhala m'kati mwamalire a dziko
lililonse.
- Aliyense ali ndi ufulu kuchoka m'dziko lililonse kuonjezerapo lake,
ndiponso kubwerera ku dziko lake.
Ndime 14
- Aliyense ali ndi ufulu kupeza mpumulo ndi kusangalala m'maiko ena m'mene
angatetezedwe ku nkhaza.
- Ufuluwu sungagwiritsidwe ntchito pa mlandu umene sukukhudza ndale, kapena
mchitidwe omwe sugwirizana ndi zolinga ndi mfundo za bungwe la mgwirizano wa
maiko (United Nations).
Ndime 15
- Aliyense ali ndi ufulu kukhala ndi mtundu.
- Palibe amene adzalandidwe mtundu wake kapena kuletsedwa kusintha mtundu
wake mosatsatira malamulo.
Ndime 16
- Amuna ndi akazi okhwima m'maganizo ndi mu msinkhu, mosaganizira mtundu,
maonkedwe a khungu kapena chipembedzo, ali ndi ufulu kukwatira kapena
kukwatiwa ndi kuyamba banja. Iwowa ali ndi ufulu, ofanana pankhani za
ukwati, pomwe ali mbanja kudzanso pothetsa banja.
- Ukwati udzamangidwa pokhapokha ngati anthu ofuna kumanga banjawo avomereza
mosakakamizidwa.
- Banja ndi lofunika kwambiri pachikhalidwe cha anthu choncho n'kofunika
kuti lipatsidwe chitetezo ndi dziko.
Ndime 17
- Aliyense ali ndi ufulu kukhala ndi katundu kapena chuma payekha kapena
mogwirizana ndi ena.
- Palibe amene adzalandidwa katundu kapena chuma mosatsatira malamulo.
Ndime 18
Aliyense ali ndi ufulu wamaganizo, chikumbumtima ndi chipembedzo; ufuluwu
ukhudzanso ufulu wotha kusintha chipembedzo kapena chikhulupiliro, ndi mtendere,
kaya payekha kapena mogwirizana ndi ena, pagulu kapena mwachinsinsi, kuonetsa
chipembedzo kapena chikhulupiliro pophunzitsa, kuchita, kupembedza ndi kutsatira
chipembedzocho.
Ndime 19
Aliyense ali ndi ufulu kuganiza ndi kulankhula, zakukhosi, ufuluwu
ukukhudzanso kukhala ndi maganizo popanda chopinga ndiponso kufufuza, kulandira
ndi kufalitsa mauthenga ndi maganizo a mtundu uliwonse kudzera pa wailesi kapena
njira ina iliyonse popanda malire.
Ndime 20
- Aliyense ali ndi ufulu kulowa bungwe lililonse ndi kusonkhana mwamtendere.
- Pasakhale munthu aliyense amene angakakamizidwe kulowa bungwe lililonse.
Ndime 21
- Aliyense ali ndi ufulu kutenga nawo mbali pa kayendetsedwe ka dziko lake,
mwa iye mwini kapena kudzera mwa nthumwi yosankhidwa mosaumirizidwa.
- Aliyense ali ndi ufulu wofanana pofuna ntchito zoyendetsedwa ndi boma
m'dziko lake.
- Chifuniro cha anthu ndicho chikhale magwero a mphamvu za boma;
chifunirochi chidzaonetsedwa pochita chisankho choona kawirikawiri chomwe
chidzakhale cha aliyense ndiponso chosakondera, ndipo chidzakhala cha
chinsinsi kapena cha njira ina iliyonse yofanana ndi iyi.
Ndime 22
Aliyense, monga m'modzi wa gulu la anthu, ali ndi ufulu kulandira chithandizo
kuchokera ku boma ndipo adzakwaniritsa izi, kudzera m'mphamvu za dziko, ndi
mgwirizano ndi maiko ena ndiponso motsatira kayendetsedwe ndi kapezedwe ka chuma
ka dziko lililonse, chithandizo cha chuma, zofunikira pa moyo ndi chikhalidwe
chake zomwe ndi mbali ya ulemu wake ndipo n'zofunika pa kakulidwe ka umunthu
wake.
Ndime 23
- Aliyense ali ndi ufulu kugwira ntchito, kusankha ntchito yomwe akufuna,
kukhala ndi zoyenereza pa ntchito, ndiponso kutetezedwa ku ulova.
- Aliyense, mopanda tsankho, ali ndi ufulu kulandira malipiro ofanana pa
ntchito yofanana.
- Aliyense amene akugwira ntchito ali ndi ufulu kulandira malipiro oyenera
otha kumupatsa iye ndi banja lake moyo wodzilemekeza ndiponso, ngati
n'kofunika, apeze njira zina zodzitetezera pa umoyo wake.
- Aliyense ali ndi ufulu kukhazikitsa kapena kulowa mabungwe a anthu ogwira
ntchito pofuna kuteteza zomupindulira zake.
Ndime 24
Aliyense ali ndi ufulu kupuma ndi kupeza msangulutso kuonjezerapo kukhala ndi
maola ogwilira ntchito oyenera ndiponso tchuthi cholipilidwa nthawi ndi nthawi.
Ndime 25
- Aliyense ali ndi ufulu kukhala ndi moyo wathanzi payekha kapena ndi banja
lake, kuonjezerapo kukhala ndi chakudya, zovala, nyumba ndi chithandizo cha
mankhwala ndi zina zofunikla pa umunthu wake, ndiponso ufulu wa chitetezo
ngati iye sali pa ntchito, akudwala, walumala, wafedwa, wakalamba, kapena
akusowa zofunika pa moyo wake pa zifukwa zimene iye sangathe kuchitapo
kanthu.
- Umayi ndi umwana uyenera kuthandizidwa ndi kusamalidwa mwapadera.
Ana onse obadwa m'banja lozindikirika mwalamulo kapena losazindikirika
adzatetezedwa umoyo wao mofanana.
Ndime 26
- Aliyense ali ndi ufulu kuphunzira. Maphunziro akhale aulele makamaka
ku pulaimale. Maphunziro a pulaimale akhale oumiliza. Maphunziro
a zaluso ndi ena akhale opezeka ndipo maphunziro apamwamba a m'makoleji
akhale opezeka kwa aliyense mofanana ndi nzeru zake.
- Maphunziro adzalinga kutukula umunthu, kulimbitsa ndi kulemekeza ufulu wa
chibadwidwe wa munthu ndi ufulu wina ofunika. Adzapititsa mtsogolo
kumvetsa, kulemekeza maganizo a anthu ena, ubale wa maiko, mtundu, kapena
magulu a zipembedzo, ndipo adzapititsa mtsogolo ntchito za bungwe la
mgwirizano wa maiko (United Nations) posungitsa bata.
- Makolo ali ndi ufulu woyamba kusankha mtundu wa maphunziro amene akufunira
ana awo.
Ndime 27
- Aliyense ali ndi ufulu kutenga nawo mbali pa zachikhalidwe cha anthu,
kusangalala ndi zaluso ndiponso kugawana za sayansi ndi phindu lake.
- Aliyense ali ndi ufulu kutetezeredwa zomupindulira zonse zomwe zili
zotsatira za ntchito ya sayansi, zolembalemba, kapena zaluso zina zomwe iye
ndi mlembi wake.
Ndime 28
Aliyense ali oyenera kukhala bata ndi mtendere pa zomuthandiza pa moyo wake
m'dziko lake ndi m'maiko mwina momwe ufulu wa chibadwidwe ndi ufulu wina
walembedwa m'chikalata chino ungakwaniritsidwe kwathunthu.
Ndime 29
- Aliyense payekha ali ndi udindo kwa anthu ena amene akukhala nawo popeza
ndi mwaiwo m'mene angathe kukwaniritsa umunthu wake kwathunthu
momasuka.
- Pokwaniritsa ufulu wake wachibadwidwe ndi ufulu wina, aliyense adzakhala
ndi malire pokhapokha malamulo atero ndi cholinga chokwaniritsa kuzindikira
ndi kulemekeza ufulu wachibadwidwe ndi ufulu wina wa ena ndiponso
kukwaniritsa chilungamo, bata ndi kukhala bwino kwa anthu m'dziko lokomera
anthu onse.
- Ufulu wa chibadwidwewu ndi ufulu wina usagwiritsidwe ntchito
mosagwirizana ndi zolinga ndi mfundo za bungwe la mgwirizano wa maiko
(United Nations).
Ndime 30
Palibe chilichonse m'chikalata chino chomwe chingatanthauziridwe kuti dziko
lililonse, gulu kapena munthu aliyense ali ndi ufulu kuchita chinthu ndi
cholinga choononga ufulu wachibadwidwe ndi ufulu wina omwe wakhazikitsidwa
m'chikalatachi.